Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 17:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Gileadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israyeli, amene ndimakhala pamaso pace, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.

2. Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,

3. Coka kuno, nutembenukire kum'mawa, ukabisale kumtsinje Keriti uli ku Yordano.

4. Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makungubwi kukudyetsa kumeneko.

5. Momwemo iye anamuka, nacita monga mwa mau a Yehova, nakakhala kumtsinje Keriti uli ku Yordano.

6. Ndipo makungubwi anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.

7. Ndipo kunacitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m'dziko.

8. Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,

9. Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Zidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse.

10. Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku cipata ca mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'cikho, ndimwe.

11. Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako.

12. Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndiribe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndirikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire odekha ndi mwana wanga, tidye, tife.

13. Ndipo Eliya anati kwa iye, Usacita mantha, kacite monga umo wanenamo, koma thanga wandiocerako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako.

14. Popeza atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzacepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi.

15. Ndipo iye anakacita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ace, masiku ambiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 17