Ndipo Eliya anati kwa iye, Usacita mantha, kacite monga umo wanenamo, koma thanga wandiocerako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako.