Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 15:16-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Israyeli masiku ao onse.

17. Ndipo Basa mfumu ya Israyeli anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asaturuke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.

18. Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golidi yense anatsala pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ciri m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ace; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabrimoni, mwana wa Hezroni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,

19. Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golidi, tiyeni lilekeke pangano liri pakati pa inu ndi Basa mfumu ya Israyeli, kuti andicokere.

20. Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ace kukathira nkhondo ku midzi ya Israyeli, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi AbeliBeti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafitali.

21. Tsono Basa atamva izi, analeka kumanga ku Rama nakhala pa Tiriza.

22. Pamenepo mfumu Asa anamemeza Ayuda onse, osatsala ndi mmodzi yense; natuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yomwe, akamange nayo Basa; ndi mfumu Asa anamangira Geba wa ku Benjamini, ndi Mizipa.

23. Ndipo macitidwe onse ena a Asa, ndi mphamvu yace yonse, ndi zonse anazicita, ndi midzi anaimanga, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda? Koma masiku a ukalamba wace anadwala mapazi ace.

24. Nagona Asa ndi makolo ace, naikidwa kwa makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; ndipo Yosafati mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.

25. Ndipo Nadabu mwana wa Yerobiamu analowa ufumu wa Israyeli caka caciwiri ca Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.

26. Nacita zoipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wace, ndi m'chimo lomwelo iye akacimwitsa nalo Aisrayeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 15