Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golidi yense anatsala pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ciri m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ace; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabrimoni, mwana wa Hezroni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,