Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 13:9-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

10. Tsono iye anayenda njira yina osabwerera njira yomweyo anaidzera pakudza ku Beteli.

11. Ndipo ku Beteli kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wace wina anadzamfotokozera macitidwe onse anawacita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo m'Beteli ndi mau ace anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao.

12. Ndipo atate wao anati kwa iwo, Wapitira njira yiti? popeza ana ace adaona njira analowera munthu wa Mulungu anacokera ku Yudayo.

13. Nanena ndi ana ace, Ndimangireni mbereko pa buru. Namangira iwo mbereko pa buru, naberekekapo iye.

14. Natsata munthu wa Mulungu, nampeza ali, tsonga patsinde pa mtengo wathundu, nanena naye, Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene uja anacokera ku Yuda? Nati, Ndine amene.

15. Tsono ananena naye, Tiye kwathu, ukadye mkate.

16. Nan iye, Sindingabwerere nawe kukalowa kwanu, kapena kudya mkate, kapena kumwa nawe madzi pano;

17. pakuti mau a Yehova anadza kwa ine, nati Usakadye mkate, kapena kumwa madzi kumeneko, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

18. Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza.

19. Tsono anabwerera naye, nakadya kwao, namwa madzi.

20. Ndipo kunacitika iwo ali cikhalire pagome, mau a Yehova anadza kwa mneneri amene anambwezayo,

21. napfuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anacokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova, Pokhala sunamvera mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira,

22. koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako.

23. Ndipo kunacitika, atadya iye mkate, ndi kumwa madzi, anammangira mbereko pa buru mneneri amene anambwezayo.

24. Ndipo atacoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha, ndipo mtembo wace unagwera m'njiramo, buru naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo.

25. Ndipo onani, anthu anapitapo naona mtembo wogwera m'njiramo, ndi mkango uli ciimire pafupi ndi mtembo, nadzanena m'mudzi m'mene munakhala mneneri wokalamba uja.

26. Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvera mau a Yehova; cifukwa cace Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo.

27. Iye nanena ndi ana ace, nati, Ndimangireni mbereko pa buru. Namangira mbereko.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 13