Ndipo ku Beteli kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wace wina anadzamfotokozera macitidwe onse anawacita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo m'Beteli ndi mau ace anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao.