Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 13:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo kunacitika, pa kumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawapfuula, kutemberera guwa la nsembe m'Beteli, Yerobiamu anatansa dzanja lace ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lace analitansira kwa iye linauma, kuti sanatha kulipfunyatitsanso.

5. Ndiponso guwalo linang'ambika, ndi phulusa la pa guwalo linatayika, monga mwa cizindikilo cimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Mulungu.

6. Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.

7. Mfumu niti kwa munthu wa Mulungu, Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso.

8. Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowa kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.

9. Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

10. Tsono iye anayenda njira yina osabwerera njira yomweyo anaidzera pakudza ku Beteli.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 13