Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 11:4-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo kunali, atakalamba Solomo, akazi ace anapambutsa mtima wace atsate milungu yina; ndipo mtima wace sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wace monga mtima wa Davide atate wace.

5. Tsono Solomo anatsata Asitoreti fano la anthu a Zidoni, ndi Milikomu fano lonyansitsa la Aamoni.

6. Ndipo Solomo anacita coipa pamaso pa Yehova, osatsata Yehova ndi mtima wonse monga Davide atate wace.

7. Pamenepo Salomo anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amoabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, pa phiri liri patsogolo pa Yerusalemu.

8. Ndipo momwemo anacitiranso akazi ace onse acilendo, amene amafukizira naphera nsembe mafano ao.

9. Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomo, pokhala mtima wace unapambuka kwa Yehova Mulungu wa Israyeli, amene adamuonekera kawiri,

10. namlamulira za cinthu comweci, kuti asatsate milungu yina; koma iye sanasunga cimene Yehova anacilamula.

11. Cifukwa cace Yehova ananena ndi Solomo, Popeza cinthu ici cacitika ndi iwe, ndipo sunasunga cipangano canga ndi malemba anga amene ndinakulamulira, zedi, ndidzakung'ambira ufumu ndi kuupatsa mnyamata wako.

12. Koma m'masiku ako sindidzatero cifukwa ca Davide atate wako, koma ndidzaung'ambira m'manja mwa mwana wako;

13. komatu sindidzacotsa ufumu wonsewo; pfuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, cifukwa ca Davide mtumiki wanga, ndi cifukwa ca Yerusalemu amene ndinamsankha.

14. Ndipo Yehova anamuutsira Solomo mdani, ndiye Hadadi M-edomu; iyeyo anali wa mbumba ya mfumu ya ku Edomu.

15. Pakuti pamene Davide adali m'Edomu, ndipo Yoabu kazembe wa nkhondo adanka kukaika akufawo, atapha amuna onse m'Edomu;

16. pakuti Yoabu ndi Aisrayeli onse anakhalako miyezi isanu ndi umodzi, mpaka atawapha amuna onse m'Edomu;

17. Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wace pamodzi naye, kumka ku Aigupto, Hadadiyo akali mwana.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 11