Cifukwa cace Yehova ananena ndi Solomo, Popeza cinthu ici cacitika ndi iwe, ndipo sunasunga cipangano canga ndi malemba anga amene ndinakulamulira, zedi, ndidzakung'ambira ufumu ndi kuupatsa mnyamata wako.