Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 10:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Seba mbiri ya Solomo yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa.

2. Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wace waukulu, ndi ngamila zakunyamula zonunkhira, ndi golidi wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomo anakamba naye zonse za m'mtima mwace.

3. Ndipo Solomo anamyankha miyambi yace yonse, panalibe kanthu kobisika ndi mfumu kamene sanamfotozera iye.

4. Ndipo pamene mfumu yaikazi ya ku Seba adaona nzeru zonse za Solomo, ndi nyumba adaimangayo,

5. ndi zakudya za pa gome lace, ndi makhalidwe a anyamata ace, ndi maimiriridwe a atumiki ace, ndi zobvala zao, ndi otenga zikho ace, ndi nsembe yace yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo.

6. Ndipo anati kwa mfumu, idali yoonadi mbiri ija ndinaimva ine ku dziko langa ya macitidwe anu ndi nzeru zanu.

7. Koma sindinakhulupira mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.

8. Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu.

9. Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wacifumu wa Israyeli; popeza Yehova anakonda Israyeli nthawi yosatha, cifukwa cace anakulongani inu ufumu, kuti mucite ciweruzo ndi cilungamo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 10