5. Ndipo mafwnu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israyeli nkhondo.
6. Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope cifukwa ca iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israyeli; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agareta ao ndi moto.
7. Ndipo Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo naye, anawadzera modzidzimutsa ku madzi a Meromu, nawagwera.
8. Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israyeli, ndipo anawakantha, nawapitikitsa mpaka ku Zidoni waukulu, ndi ku MiseripotuMaimu, ndi ku cigwa ca Mizepe kum'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyira ndi mmodzi yense.
9. Ndipo Yoswa anawacitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magareta ao ndi moto.
10. Ndipo Yoswa anabwerera m'mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yace ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukuru wa maufumu aja onse.
11. Ndipo anakantha amoyo onse anali m'mwemo, ndi lupanga lakuthwa, ndi kuwaononga konse, osasiyapo ndi mmodzi yense wakupuma mpweya; ndipo anatentha Hazori ndi moto.
12. Ndipo Yoswa analanda midzi yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira.
13. Koma midzi yonse yomangidwa pa zitunda zao Israyeli sanaitentha, koma wa Hazori wokha; wnenewu Yoswa anautentha.
14. Ndi zofunkha zonse za midzi iyi ndi ng'ombe ana a Israyeli anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya.