13. Abzyala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, cifukwa ca mkwiyo woopsya wa Yehova.
14. Atero Yehova ponenera anansi anga onse oipa, amene akhudza colowa cimene ndalowetsamo anthu anga Israyeli; taonani, ndidzazula iwo m'dziko lao, ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pao.
15. Ndipo padzakhala kuti nditazula iwo, ndidzabwera, ndipo ndidzawacitira cisoni; ndipo ndidzabwezanso iwo, yense ku colowa cace, ndi yense ku dziko lace.
16. Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.
17. Koma ngati sakumva, ndidzazula mtundu umene wa anthu, kuuzula ndi kuuononga, ati Yehova.