30. Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa capacifuwa ca ciweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula ciweruzo ca ana a Israyeli pamtima pace pamaso pa Yehova kosalekeza.
31. Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha.
32. Ndipo polowa mutu pakhale pakati pace; pakhale mkawo pozungulira polowa pace, wa nchito yoomba, ngati polowa pa malaya ociniiriza, pangang'ambike.
33. Ndipo pa mbinyiru wace upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiirira, pambinyiru pace pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolidi pozungulira;
34. mliu wagolidi ndi khangaza, mliu wagolidi ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira.
35. Ndipo Aroni aubvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lace pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakuturuka iye, kuti asafe.
36. Ndipo upange golidi waphanthiphanthi woona, ndi kulocapo, monga malocedwe a cosindikizira. KUPATULIKIRA YEHOVA.
37. Nuciike pamkuzi wamadzi, ndipo cikhale panduwira, cikhale patsogolo pace pa nduwira.
38. Ndipo cizikhala pamphumi pace pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israyeli azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo cizikhala pamphumi pace kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova.
39. Ndipo upikule maraya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika.
40. Ndipo usokere ana a Aroni maraya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma.
41. Ndipo ubveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ace omwe; ndi a kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andicitire Ine nchito ya nsembe.
42. Uwasokerenso zobvala za miyendo za bafuta wa thome losansitsa kubisa marisece ao; ziyambire m'cuuno zifikire kuncafu.
43. Ndipo azibvale Aroni, ndi ana ace, pakulowa iwo ku cihema cokomanako, kapena poyandikiza iwo ku guwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zace pambuyo pace.