1. Ndipo anamuka munthu wa banja la Levi, natenga mwana wamkazi wa Levi.
2. Ndipo anaima mkaziyo, naonamwanawamwamuna; m'mene anamuona kuti ali wokoma, anambisa miyezi itatu.
3. Koma pamene sanathe kumbisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa nyanja.
4. Ndipo mlongo wace anaima patali, adziwe comwe adzamcitira.
5. Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ace anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wace akatenge.
6. Pamene anakabvundukula, anapenya mwanayo; ndipo, taonani, khandalo lirikulira. Ndipo anamva naye cifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri.