Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ace anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wace akatenge.