Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yuda 1:5-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwaturutsa m'dziko La Aigupto, anaononganso iwo osakhulunirira.

6. Angelonso amene sanasunga cikhalidwe cao coyamba, komatu anasiya pokhala pao pao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira ciweruziro ca tsiku lalikuru.

7. Monga; Sodoma ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kursara zilakolako zacilendo, iikidwa citsanzo, pakucitidwa cilango ca mota wosatha.

8. Momwemonso iwo m'kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nacitira mwano maulemerero.

9. Koma Mikayeli mkulu wa angelo, pakucita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumehulira cifukwa comcitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.

10. Koma iwowa zimene sazidziwa azicitira mwano; ndipo zimene azizindikira cibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika,

11. Tsoka kwa iwo! pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'cisokero ca Balamu cifukwa ca kulipira, natayika m'citsutsano ca Kore,

12. Iwo ndiwo okhala mawanga pa mapwando anu a cikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawid, yozuka mizu;

13. mafunde oopsya a nyanja, akuwinduka thobvu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.

14. Ndipo kwa iwo, Henoke, wacisanu ndi ciwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ace zikwi makumi,

Werengani mutu wathunthu Yuda 1