Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yuda 1:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. YUDA, kapolo wa Yesu Kristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Kristu:

2. Cifundo ndi mtendere ndi cikondi zikucurukireni.

3. Okondedwa, pakucira cangu conse cakukulemberani za cipulumutso ca ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu cifukwa ca cikhulupiriro capatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.

4. Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira citsutso ici, anthu osapembedza, akusandutsa cisomo ca Mulungu wathu cikhale cilak olako conyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Kristu.

5. Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwaturutsa m'dziko La Aigupto, anaononganso iwo osakhulunirira.

6. Angelonso amene sanasunga cikhalidwe cao coyamba, komatu anasiya pokhala pao pao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira ciweruziro ca tsiku lalikuru.

7. Monga; Sodoma ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kursara zilakolako zacilendo, iikidwa citsanzo, pakucitidwa cilango ca mota wosatha.

8. Momwemonso iwo m'kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nacitira mwano maulemerero.

9. Koma Mikayeli mkulu wa angelo, pakucita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumehulira cifukwa comcitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.

10. Koma iwowa zimene sazidziwa azicitira mwano; ndipo zimene azizindikira cibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika,

11. Tsoka kwa iwo! pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'cisokero ca Balamu cifukwa ca kulipira, natayika m'citsutsano ca Kore,

Werengani mutu wathunthu Yuda 1