Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 8:24-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.

25. Pamenepo anaikanso manja m'maso mwace; ndipo anapenyetsa, naciritsidwa, naona zonse mbee.

26. Ndipo anamtumiza amuke kwao, nanena, Usalowe konse m'mudzi.

27. Ndipo anaturuka Yesu, ndi ophunzira ace, nalowa ku midzi ya ku Kaisareya wa Filipi; ndipo panjira anafunsa ophunzira ace, nanena nao, Kodi anthu anena kuti Ine ndine yani?

28. Ndipo ananena, nati, Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri.

29. Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, Ndinu Kristu.

30. Ndipo anawauzitsa iwo kuti asanene kwa munthu mmodzi za Iye.

31. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akuru ndi ansembe akulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkuca wace akauke.

32. Ndipo mauwo ananena poyera. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula.

33. Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ace, namdzudzula Petro, nanena, Coka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.

34. Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ace, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wace, nanditsate Ine.

35. Pakuti yense wakufuna kupulumutsa moyo wace adzautaya; ndipo yense wakutaya moyo wace cifukwa ca Ine, ndi cifukwa ca Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.

36. Pakuti munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wace?

37. Pakuti munthu akapereka ciani cosintha naco moyo wace?

38. Pakuti yense wakucita manyazi cifukwa ca Ine, ndi ca mau anga mu mbadwo uno wacigololo ndi wocimwa, Mwana wa munthu adzacitanso manyazi cifukwa ca iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ace oyera, mu ulemerero wa Atate wace.

Werengani mutu wathunthu Marko 8