Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 6:21-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwace kwa Herode, iye anawakonzera phwando akuru ace ndi akazembe ace ndi anthu omveka a ku Galileya;

22. ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiya analowa yekha nabvina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pacakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine ciri conse ucifuna, ndidzakupatsa iwe.

23. Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Ciri conse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga.

24. Ndipo anaturuka, nati kwa amace, Ndidzapempha ciani? Ndipo iyel anati, Mutu wace wa Yohane Mbatizi.

25. Ndipo pomwepo analowa m'mangu m'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wace wa Yohane Mbatizi mumbizi.

26. Ndipo mfumu inamva cisoni cacikuru; koma cifukwa ca malumbiro ace, ndi ca iwo akukhala pacakudya, sanafuna kumkaniza.

27. Ndipo pomwepo mfumu inatuma mnyamata, namlamulira akatenge mutu wace; ndipo iye anamuka namdula mutu m'nyumba yandende;

28. natengera mutu wace mumbizi, naupereka kwa buthulo; ndipo buthu linaupereka kwa amace.

29. Ndipo m'mene ophunzira ace anamva, anadza nanyamula mtembo wace nauika m'manda.

30. Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza ziri zonse adazicita, ndi zonse adaziphunzitsa,

31. Ndipo Iye ananena nao, Idzani inu nokha padera ku malo acipululu, mupumule kamphindi, Pakuti akudza ndi akucoka anali piringu piringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.

32. Ndipo anacokera m'ngalawa kunka ku malo acipululu padera.

33. Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikila, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ocokera m'midzi monse, nawapitirira.

34. Ndipo anaturuka Iye, naona khamu lalikuru la anthu, nagwidwa cifundo ndi iwo, cifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.

35. Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ace, nanena, Malo ana nga cipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu;

36. muwauze kuti amuke, alowe kumiraga ndi ku midzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya.

37. Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya?

38. Ndipo Iye ananena nao, kuti, Muli nayo mikate ingati? pitani, mukaone. Ndipo m'mene anadziwa ananena, lsanu, ndi nsomba ziwiri.

Werengani mutu wathunthu Marko 6