Ndipo anaturuka Iye, naona khamu lalikuru la anthu, nagwidwa cifundo ndi iwo, cifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.