ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiya analowa yekha nabvina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pacakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine ciri conse ucifuna, ndidzakupatsa iwe.