Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 12:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wamphesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.

2. Ndipo m'nyengo yace anatuma kapolo kwa olimawo, kuti alandireko kwa olimawo zipatso za m'munda wamphesa.

3. Ndipo iwo anamtenga iye, nampanda, namcotsa wopanda kanthu.

4. Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namcitira zomcititsa manyazi.

5. Ndipo anatuma wina; iyeyu anamupha; ndi ena ambiri; ena anawapanda, ndi ena anawapha.

6. Anamtsalira mmodzi, ndiye mwana wace wokondedwa; potsiriza anamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamcitira ulemu mwana wanga.

7. Koma olima ajawo, ananena mwa iwo okha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu.

8. Ndipo anamtenga, namupha iye, namtaya kunja kwa munda.

9. Pamenepo mwini munda adzacita ciani? Adzafika, nadzaononga olimawo, nadzapereka mundawo kwa ena.

10. Kodi simunawerenga ngakhale lembo ili;Mwala umene anaukana omanga nyumba,Womwewu unayesedwa mutu wa pangondya:

11. Ici cinacokera kwa Ambuye, Ndipo ciri cozizwitsa m'maso mwathu?

12. Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nacoka.

13. Ndipo anatuma kwa Iye ena a Afarisi ndi a Aherode, kuti akamkole Iye m'kulankhula kwace.

14. Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?

15. Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa cinyengo cao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.

Werengani mutu wathunthu Marko 12