Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 21:12-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma pamene tinamva izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko, asakwere iye kunka ku Yerusalemu.

13. Pamenepo Paulo anayankha, Mucitanji, polira ndi kundiswera mtima? pakuti ndakonzeka Ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu cifukwa ca dzina la Ambuye Yesu.

14. Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kucitidwe.

15. Ndipo atapita masiku awa tinakonza akatundu athu, ntikwera ku Yerusalemu.

16. Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kaisareya, natenganso wina Mnaso wa ku Kupro, wophunzira wakale, amene adzaticereza.

17. Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale anatilandira mokondwera.

18. Ndipo m'mawa mwace Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo.

19. Ndipo atawalankhula iwo, anawafotokozera cimodzi cimodzi zimene Mulungu anacita kwa amitundu mwa utumiki wace.

20. Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupira; ndipo ali naco cangu onsewa, ca pa cilamulo;

21. ndipo anamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a ku amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana ao, kapena asayende monga mwa miyambo.

22. Nciani tsono? adzamva ndithu kuti wafika.

23. Cifukwa cace ucite ici tikuuza iwe; tiri nao amuna anai amene anawinda;

24. amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kati amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzacabe, koma kuti iwe wekhaoso uyenda molunjika, nusunga cilamulo.

25. Kama kunena za amitundu adakhulupirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.

26. Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwace m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa m'Kacisi, nauza cimarizidwe ca masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.

27. Ndipo pamene masiku asanu, ndi awiri anati amarizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye m'Kacisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,

28. napfuula, Amuna a Israyeli, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi cilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Ahelene nalowa nao m'Kacisi, nadetsa malo ana oyera.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 21