Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 21:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Ko, ndi m'mawa mwace ku Rode, ndipo pocokerapo ku Patara;

2. ndipo m'mene tinapeza ngalawa Yakuoloka kunka ku Foinike, tinalowamo, ndi kupita nayo.

3. Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kupro, tinacisiya kulamanzere, ntinapita ku Suriya; ndipo tinakoceza ku Turo; pakuti pamenepo ngalawainafuna kutula akatundu ace.

4. Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masikuasanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu.

5. Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidacoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana anatiperekeza kufikira kuturuka m'mudzi; ndipo pogwadira pa mcenga wa kunyanja, tinapemphera,

6. ndi kulawirana; ndipo tinalowa m'ngalawa, koma iwo anabwera kwao.

7. Ndipo ife titatsiriza ulendo wathu wocokera ku Turo, tinafika ku Ptolemayi; ndipo m'mene tidalankhula abale, tinakhala nao tsiku limodzi.

8. Ndipo m'mawa mwace tinacoka, ntinafika ku Kaisareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.

9. Ndipo munthuyu anali nao ana akazi anai, anamwali, amene ananenera.

10. Ndipo pokhalapo masiku ambiri, anatsika ku Yudeya mneneri, dzina lace Agabo.

11. Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a m'Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu.

12. Koma pamene tinamva izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko, asakwere iye kunka ku Yerusalemu.

13. Pamenepo Paulo anayankha, Mucitanji, polira ndi kundiswera mtima? pakuti ndakonzeka Ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu cifukwa ca dzina la Ambuye Yesu.

14. Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kucitidwe.

15. Ndipo atapita masiku awa tinakonza akatundu athu, ntikwera ku Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 21