Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 19:3-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'ciani? Ndipo anai, Mu ubatizo wa Yohane.

4. Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire iye amene adzadza pambuyo pace, ndiye Yesu.

5. Pamene anamva ici, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.

6. Ndipo pamene Paulo anaika manja ace pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.

7. Onsewo anali ngati amuna khumi ndi awiri.

8. Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.

9. Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawacokera, napatutsa akuphunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Turano.

10. Ndipo anacita comweco zaka ziwiri; kotero kuti onseakukhala m'Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Ahelene.

11. Ndipo Mulungu anacita zamphamvu za pa zokha ndi manja a Paulo;

12. kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsaru zopukutira ndi za panchito, zocokera pathupi pace, ndipo nthenda zinawacokera, ndi mizimu yoipa inaturuka.

13. Koma Ayuda enanso oyendayenda, oturutsa ziwanda, anadziyesa kuchula pa iwo amene anali ndi mizimu yoipa dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo.

14. Ndipo panali ana amuna asanu ndi awiri a Skeva, Myuda, mkuru wa ansembe amene anacita ici.

15. Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?

16. Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amarisece ndi olasidwa.

17. Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Ahelene, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Yesu Iinakuzika.

18. Ndipo ambiri a iwo akukhulipirawo anadza, nabvomereza, nafotokoza macitidwe ao.

19. Ndipo ambiri a iwo akucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wace, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 19