Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 18:4-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo anafotokozera m'sunagogemasabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.

5. Koma pamene Sila ndi Timoteo anadza potsika ku Makedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nacitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Kristu.

6. Koma pamene iwo anamkana, nacita mwano, anakutumula maraya ace, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndiribe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.

7. Ndipo anacoka kumeneko, nalowa m'nyumba ya munthu, dzina lace Tito Yusto, amene anapembedza Mulungu, nyumba yace inayandikizana ndi sunagoge.

8. Ndipo Krispo, mkuru wasunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ace onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupira, nabatizidwa.

9. Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale cete;

10. cifukwa Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; cifukwa ndiri nao anthu ambiri m'mudzi muno.

11. Ndipo anakhala komwe caka cimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsamau a Mulungu mwa iwo.

12. Tsono pamene Galiyo anali ciwanga ca Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye ku mpando wa ciweruziro,

13. kuti, Uyu akopa anthu apembedze Mulungu pokana cilamulo.

14. Koma pamene Paulo anati atsegule pakamwa pace, Galiyo anati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa cosalungama, kapena dumbo loipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu;

15. koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi cilamulo canu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.

16. Ndipo anawapitikitsa pa mpando wa ciweruziro.

17. Ndipo anamgwira Sostene, mkuru wa sunagoge, nampanda ku mpando wa ciweruziro. Ndipo Galiyo sanasamalira zimenezi.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 18