Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 18:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitapita izi anacoka ku Atene, nadza ku Korinto.

2. Ndipo anapeza Myuda wina dzina lace Akula, pfuko lace la ku Ponto, atacoka catsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wace Priskila, cifukwa Klaudiyo analamulira Ayuda onse acoke m'Roma; ndipo Pauloanadza kwa iwo:

3. ndipo popeza anali wa nchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira nchito; pakuti nchito yao inali yakusoka mahema.

4. Ndipo anafotokozera m'sunagogemasabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.

5. Koma pamene Sila ndi Timoteo anadza potsika ku Makedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nacitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Kristu.

6. Koma pamene iwo anamkana, nacita mwano, anakutumula maraya ace, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndiribe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.

7. Ndipo anacoka kumeneko, nalowa m'nyumba ya munthu, dzina lace Tito Yusto, amene anapembedza Mulungu, nyumba yace inayandikizana ndi sunagoge.

8. Ndipo Krispo, mkuru wasunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ace onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupira, nabatizidwa.

9. Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale cete;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 18