Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 17:2-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo Paulo, monga amacita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira,

3. natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Kristu.

4. Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Sila; ndi Ahelene akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akuru osati owerengeka.

5. Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa acabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nacititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira ku nyumba ya Yasoni, nafuna kuwaturutsira kwa anthu.

6. Pamene sanawapeza anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akuru a mudzi, napfuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;

7. amene Yasoni walandira; ndipo onsewo acita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu yina, Yesu.

8. Ndipo anabvuta anthu, ndi akuru a mudzi, pamene anamva zimenezi.

9. Ndipo pamene analandira cikole kwa Yasoni ndi enawo, anawamasula.

10. Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Sila usiku kunka ku Bereya; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda.

11. Amenewa anali mfulu koposa a m'Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.

12. Ndipo ambiri a iwo anakhulupira; ndi akazi a Cihelene omveka, ndi amuna, osati owerengeka.

13. Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereyanso, anadza komwekonso, nautsa, nabvuta makamu.

14. Pomwepo abale anaturutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Sila ndi Timoteo anakhalabe komweko.

15. Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Sila ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi cangu conse, anacoka.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 17