Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 16:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. pocokera kumeneko tinafika ku Filipi, mudzi wa ku Makedoniya, waukuru wa m'dzikomo, wa miraga ya Roma; ndipojidagona momwemo masiku ena.

13. Tsiku la Sabata tinaturuka kumudzi kunka ku mbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana,

14. Ndipo anatimva mkazi wina dzina lace Lidiya, wakugulitsa cibakuwa, wa ku mudzi wa Tiyatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wace Ambuye anatsegula, kuti amvere zimene anazinena Paulo.

15. Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pace anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.

16. Ndipo panali, pamene tinalinkunka kukapemphera, anakomana ndi ife namwali wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ace zambiri pakubwebweta pace.

17. Ameneyo anatsata Paulo ndi ite, napfuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba amene akulalikirani inu njira ya cipulumutso.

18. Ndipo anacita cotero masiku ambiri. Koma Paulo anabvutika mtima ndithu, naceuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Kristu, turuka mwa iye. Ndipo unaturuka nthawi yomweyo.

19. Koma pamene ambuye ace anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Sila, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akuru,

20. ndipo pamene adanka nao kwa oweruza, anati, Anthu awa abvuta kwambiri mudzi wathu, ndiwo Ayuda,

21. ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuicita, ndife Aroma.

22. Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira maraya ao; nalamulira kuti awakwapule.

23. Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.

24. Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m'cipinda ca m'kati, namangitsa mapazi ao m'zigologolo.

25. Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Sila analinkupemphera, nayimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 16