Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 12:8-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'cuuno, numange nsapato zako. Nacita cotero. Ndipo ananena naye, Pfunda cobvala cako, nunelitsate ine.

9. Ndipo anaturuka, namtsata; ndipo sanadziwa kuti ncoona cocitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.

10. Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi paciwiri, anadza ku citseko cacitsulo cakuyang'ana kumudzi; cimene cidawatsegukira cokha; ndipo anaturuka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamcokera.

11. Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wace nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku cilingiriro conse ca anthu a Israyeli.

12. Ndipo m'mene adalingirirapo, anadza ku nyumba ya Marlys amace wa Yohane wonenedwanso Marko; pamenepo ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo analikupemphera,

13. Ndipo m'mene anagogoda pa citseko ca pakhomo, linadza kudzabvomera buthu, dzina lace Roda.

14. Ndipo pozindikira mau ace a Petro, cifukwa ca kukondwera sanatsegula pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo.

15. Koma anati kwa iye, Wamisala iwe. Ndipo analimbika ndi kunena kuti nkutero. Ndipo ananena, Ndiye mngelo wace.

16. Koma Petro anakhala cigogodere; ndipo m'mene adamtsegulira, anamuona iye, nadabwa.

17. Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale cete, anawafotokozera umo, adamturutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi, Ndipo anaturuka napita kwina.

18. Koma kutaca, panali phokoso lalikuru mwa asilikari, Petro wamuka kuti.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 12