Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 11:16-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.

17. Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Kristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?

18. Ndipo pamene anamva izi, anakhala du, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, a Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.

19. Pamenepo iwotu, akubalalika cifukwa ca cisautsoco cidadza pa Stefano, anafikira ku Foinike, ndi Kupro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha.

20. Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kupro, ndi Kurene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Ahelene, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.

21. Ndipo dzanja la Ambuye linali nao; ndi unyinji wakukhulupira unatembenukira kwa Ambuye.

22. Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala m'Yerusalemu; ndipo anatuma Bamaba apite kufikira ku Antiokeya;

23. ameneyo, m'mene anafika, naona cisomo ca Mulungu, anakondwa; ndipo anawandandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;

24. cifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi cikhulupiriro: ndipo khamu lalikuru lidaonjezeka kwa Ambuye.

25. Ndipo anaturuka kunka ku Tariso kufunafuna Saulo;

26. ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti caka conse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kuchedwa Akristu ku Antiokeya.

27. Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya.

28. Ndipo anyanamuka mmodzi wa iwo, dzina lace Agabo, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudiyo.

29. Ndipo akuphunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m'Yudeya;

30. iconso anacita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Bamaba ndi Saulo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 11