Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m'mene muturuka m'mudzi womwewo, sansani pfumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo.

6. Ndipo iwo anaturuka, napita m'midzi m'midzi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, ndi kuciritsa ponse.

7. Ndipo Herode ciwangaco anamva mbiri yace ya zonse zinacitika; ndipo inamthetsa nzeru, cifukwa ananena anthu ena, kuti Yohane anauka kwa akufa;

8. koma ena, kuti Eliya anaoneka; ndipo ena, kuti mneneri wina wa akale aja anauka.

9. Ndipo Herode anati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo anafunafuna kumuona iye.

10. Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera iye zonse anazicita. Ndipo iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka ku mudzi dzina lace Betsaida.

11. Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, naciritsa amene anasowa kuciritsidwa.

12. Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite ku midzi yoyandikira ndi kumiraga, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; cifukwa tiri ku malo acipululu kuno.

13. Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tiribe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

Werengani mutu wathunthu Luka 9