Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:13-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tiribe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

14. Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma iye anati kwa ophunzira ace, Khalitsani iwo pansi magulu magulu, ngati makumi asanu asanu.

15. Ndipo anatero, nawakhalitsa pansi onsewo.

16. Ndipo iye, m'mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang'ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo.

17. Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, mitanga khumi ndi iwiri.

18. Ndipo kunali, pamene iye analikupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani?

19. Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.

20. Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Kristu wa Mulungu.

21. Ndipo iye anawauzitsa iwo, nalamulira kuti asanene ici kwa munthu ali yense;

22. nati, Kuyenera kuti Mwana wa munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akuru, ndi ansembe akuru, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lacitatu.

23. Ndipo iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wace tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.

24. Pakutiamene ali yense akafuna kupulumutsa moyo wace, iye adzautaya; koma amene ali yense akataya moyo wace cifukwa ca Ine, iye adzaupulumutsa uwu.

25. Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wace?

26. Pakuti amene ali yense: adzacita manyazi cifukwa ca Ine ndi mau anga, Mwana wa munthu adzacita manyazi cifukwa ca iye, pamene adzafika ndi ulemerero wace ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera.

27. Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.

28. Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera.

29. Ndipo m'kupemphera kwace, maonekedwe a nkhope yace anasandulika, ndi cobvala cace cinayera ndi kunyezimira.

Werengani mutu wathunthu Luka 9