Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite ku midzi yoyandikira ndi kumiraga, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; cifukwa tiri ku malo acipululu kuno.

13. Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tiribe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

14. Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma iye anati kwa ophunzira ace, Khalitsani iwo pansi magulu magulu, ngati makumi asanu asanu.

15. Ndipo anatero, nawakhalitsa pansi onsewo.

16. Ndipo iye, m'mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang'ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo.

17. Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, mitanga khumi ndi iwiri.

Werengani mutu wathunthu Luka 9