Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 8:4-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo pamene khamu lalikuru la anthu linasonkhana, ndi anthu a ku midzi yonse anafika kwa iye, anati mwa fanizo:

5. Anaturuka wofesa kukafesa mbeu zace; ndipo m'kufesa kwace zina zinagwa m'mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m'mlengalenga zinatha kuzidya.

6. Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, cifukwa zinalibe mnyontho.

7. Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inapuka pamodzi nazo, nizitsamwitsa.

8. Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena iye izi anapfuula, iye amene ali ndi makutu akumva amve.

9. Ndipo ophunzira ace anamfunsa Iye, kuti, Fanizo ili liri lotani?

10. Ndipo iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse,

11. Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu,

12. Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nacotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.

13. Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.

14. Ndipo zija zinagwa ku mingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi cuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.

15. Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

16. Ndipo palibe munthu, atayatsa, nyali, aibvundikira ndi cotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pacoikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.

17. Pakuti palibe cinthu cobisika, cimene sicidzakhala coonekera; kapena cinsinsi cimene sicidzadziwika ndi kubvumbuluka.

Werengani mutu wathunthu Luka 8