Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 8:32-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zirinkudya m'phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola.

33. Ndipo ziwandazo zinaturuka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.

34. Ndipo akuwetawo m'mene anaona cimene cinacitika, anathawa, nauza a kumudzi ndi kumiraga yace.

35. Ndipo iwo anaturuka kukaona cimene cinacitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinaturuka mwa iye, alikukhala pansi ku mapazi ace a Yesu wobvala ndi wa nzeru zace; ndipo iwo anaopa.

36. Ndipo amene anaona anawauza iwo maciritsidwe ace a wogwidwa ciwandayo.

37. Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa Ioyandikira anamfunsa iye acoke kwa iwo; cifukwa anagwidwa ndi mantha akuru. Ndipo iye analowa m'ngalawa, nabwerera.

38. Ndipo munthuyo amene ziwanda zinaturuka mwa iye anampempha iye akhale ndi iye; koma anamuuza apite, nanena,

39. Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuruzo anakucitira iwe Mulungu. Ndipo iye anacoka, nalalikira ku mudzi wonse zazikuruzo Yesu anamcitira iye,

40. Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira iye; pakuti onse analikumlindira iye.

41. Ndipo onani, panadza munthu dzina lace Yairo, ndipo iye ndiye mkuru wa sunagoge; ndipo anagwa pamapazi ace a Yesu, nampempha iye adze kunyumba kwace;

42. cifukwa anali naye mwana wamkazi mmodzi yekha, wa zaka zace ngati khumi ndi ziwiri, ndipo analinkumwalira iye, Koma pakupita iye anthu a mipingo anakanikizana naye,

43. Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yacidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wace zonse, ndipo sanathe kuciritsidwa ndi mmodzi yense,

44. anadza pambuyo pace, nakhudza mphonje yacobvala cace; ndipo pomwepo nthenda yace inaleka.

45. Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana.

46. Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti a ndazindikira Ine kuti mphamvu yaturuka mwa Ine.

47. Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisika, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pace, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo cifukwa cace ca kumkhudza iye, ndi kuti anaciritsidwa pomwepo.

48. Ndipo iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

49. M'mene iye anali cilankhulire, anadza wina wocokera kwa mkuru wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usambvute Mphunzitsi.

50. Koma Yesu anamva, namyankha, kuti, Usaope; khulupira kokha, ndipo iye adzapulumutsidwa.

51. Ndipo pakufika iye kunyumbako, sanaloleza wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amace.

Werengani mutu wathunthu Luka 8