Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 8:27-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo ataturuka pamtanda iye, anakomana naye mwamuna wa kumudzi, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanabvala cobvala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda.

28. Ndipo pakuona Yesu, iye anapfuula, nagwa pansi pamaso pace, nati ndi mau akuru, Ndiri naco ciani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkurukuru? Ndikupemphani Inu musandizunze.

29. Pakuti iye adalamula mzimu wonyansa uturuke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi ciwandaco kumapululu.

30. Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, cifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.

31. Ndipo zinampempha iye, kuti asazilamulire zicoke kulowa kuphompho.

32. Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zirinkudya m'phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola.

33. Ndipo ziwandazo zinaturuka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.

34. Ndipo akuwetawo m'mene anaona cimene cinacitika, anathawa, nauza a kumudzi ndi kumiraga yace.

35. Ndipo iwo anaturuka kukaona cimene cinacitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinaturuka mwa iye, alikukhala pansi ku mapazi ace a Yesu wobvala ndi wa nzeru zace; ndipo iwo anaopa.

36. Ndipo amene anaona anawauza iwo maciritsidwe ace a wogwidwa ciwandayo.

37. Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa Ioyandikira anamfunsa iye acoke kwa iwo; cifukwa anagwidwa ndi mantha akuru. Ndipo iye analowa m'ngalawa, nabwerera.

Werengani mutu wathunthu Luka 8