Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 7:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera akuru anga, ndiri nao asilikari akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tacita ici, nacita.

9. Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeza, ngakhale mwa Israyeli, cikhulupiriro cacikuru cotere.

10. Ndipo pakubwera ku nyumba otumidwawo, anapeza kapoloyo wacira ndithu.

11. Ndipo kunali, katapita kamphindi, iye ana pita kumudzi, dzina lace Nayini; ndipo ophunzira ace ndi mpingo waukuru wa anthu anapita nave.

12. Ndipo pamene anayandikira ku cipata ca mudziwo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amace ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri a kumudzi anali pamodzi naye.

13. Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi cifundo cifukwa ca iye, nanena naye, Usalire.

14. Ndipo anayandikira, nakhudza cithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.

15. Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amace.

Werengani mutu wathunthu Luka 7