Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 7:15-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amace.

16. Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkuru wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzaceza ndi anthu ace.

17. Ndipo mbiri yace imeneyo inabuka ku Yudeya lonse, ndi ku dziko lonse loyandikira.

18. Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza iye zonsezi.

19. Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ace, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?

20. Ndipo pakufika kwa iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?

21. Nthawi yomweyo iye anaciritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zobvuta, ndi mizimu yoipa; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.

22. Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.

23. Ndipo wodala iye amene sakhomudwa cifukwa ca Ine.

24. Ndipo atacoka amithenga ace a Yohane, iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munaturuka kunka kucipululu kukapenya ciani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

Werengani mutu wathunthu Luka 7