Ndipo atacoka amithenga ace a Yohane, iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munaturuka kunka kucipululu kukapenya ciani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?