Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 6:37-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. Ndipo 5 musawatsutsa, ndipo simudzatsutsidwa. Masulani, ndipo mudzamasulidwa.

38. 6 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti 7 kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

39. Ndipo iye ananenanso nao fanizo, 8 Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzace wakhungu? kodi sadzagwa onse awiri m'mbuna?

40. 9 Wophunzira saposa mphunzitsi wace; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wace.

41. Ndipo uyang'aniranji kacitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira?

42. 10 Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndicotse kacitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! thanga wacotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kucotsa kacitsotso ka m'diso la mbale wako.

43. Pakuti 11 palibe mtengo wabwino wakupatsa zipatso zobvunda; kapenanso mtengo woipa wakupatsa zipatso zabwino,

44. Pakuti 12 mtengo uli wonse uzindikirika ndi cipatso cace. Pakuti anthu samachera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samachera mphesa,

45. 13 Munthu wabwino aturutsa zabwino m'cuma cokoma ca mtima wace; ndi munthu woipa aturutsa zoipa m'coipa cace: pakuti m'kamwa mwace mungolankhula mwa kucuruka kwa mtima wace.

46. Ndipo 14 mundichuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusacita zimene ndizinena?

47. 15 Munthu ali yense wakudza kwa Ine, ndi kumva mau anga, ndi kuwacita, ndidzakusonyezani amene afanana naye.

48. Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza cigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunakhoza kuigwedeza; cifukwa idamangika bwino.

Werengani mutu wathunthu Luka 6