Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 5:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuti cizizwo cidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola;

10. ndipo cimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene anali anzace a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.

11. Ndipo m'mene iwo anakoceza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata iye.

12. Ndipo panali, pamene iye anali m'mudzi wina, taona, munthu wodzala ndikhate; ndipopameneanaona Yesu, anagwa nkhope yace pansi, nampempha iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.

13. Ndipo iye anatambalitsa dzanja lace, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka, Ndipo pomwepo khate linacoka kwa iye.

14. Ndipo iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu ali yense; koma ucoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa cikonzedwe cako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.

15. Koma makamaka mbiri yace ya iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhanakudzamvera, ndi kudzaciritsidwa nthenda zao.

16. Koma iye anazemba, nanka m'mapululu, nalikupemphera.

17. Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene anacokera ku midzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi iye yakuwaciritsa,

18. Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa iye.

Werengani mutu wathunthu Luka 5