Ndipo iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu ali yense; koma ucoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa cikonzedwe cako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.