Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 5:17-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene anacokera ku midzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi iye yakuwaciritsa,

18. Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa iye.

19. Ndipo posapeza polowa naye, cifukwa ca unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa chindwi, namtsitsira iye poboola pa chindwi ndi kama wace, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.

20. Ndipo iye, pakuona cikhulupiriro cao, anati, Munthu iwe, macimo ako akhululukidwa.

21. Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, ndani Uyu alankhula zomcitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira macimo, koma Mulungu yekha?

22. Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m'mitima yanu?

23. Capafupi nciti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe macimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende?

24. Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nayo mphamvu pa dziko lapansi yakukhululukira macimo, (anati iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.

25. Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza cimene adagonapo, nacokapo, kunka kunyumba kwace, wakulemekeza Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Luka 5