Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 4:6-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo mdierekezi anati kwa iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: cifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna.

7. Cifukwa cace ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.

8. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,Ambuye Mulungu wako uzimgwadira,Ndipo iye yekha yekha uzimtumikira,

9. Ndipo anamtsogolera iye ku Yerusalemu, namuika iye pamwamba pa cimbudzi ca Kacisiyo, nati kwa iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi;

10. pakuti kwalembedwa, kuti,Adzalamulira angelo ace za, iwe, kuti akucinjirize,

11. Ndipo,Pa manja ao adzakunyamula iwe,Kuti ungagunde konse phazi lako pamwala,

12. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa,Usamuyese Ambuye Mulungu wako,

13. Ndipo mdierekezi, m'mene adamariza mayesero onse, analekana naye kufikira nthawi yina.

14. Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yace ya iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.

15. Ndipo iye anaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalemekezedwa ndi anthu onse.

16. Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.

17. Ndipo anapereka kwa iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m'mene iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa,

18. Mzimu wa Ambuye uli paine,Cifukwa cace iye anandidzozaIne ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino:Anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe,Ndi akhungu kuti apenyenso,Kuturutsa ndi ufuru ophwanyika,

19. Kulalikira caka cosankhika ca Ambuye.

20. Ndipo m'mene iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa iye.

21. Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu.

Werengani mutu wathunthu Luka 4