Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 4:20-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo m'mene iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa iye.

21. Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu.

22. Ndipo onse anamcitira iye umboni nazizwa ndi mau a cisomo akuturuka m'kamwa mwace; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?

23. Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadziciritsa wekha: zonse zija tazimva zinacitidwa ku Kapernao, muzicitenso zomwezo kwanu kuno.

24. Ndipo iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika ku dziko la kwao.

25. Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri m'lsrayeli masiku ace a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikuru pa dziko lonselo;

26. ndipo Eliya sanatumidwa kwa mmodzi wa iwo, koma ku Sarepta wa ku Sidoniya, kwa mkazi wamasiye.

27. Ndipo munali akhate ambiri m'Israyeli masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Namani yekha wa ku Suriya.

28. Ndipo onse a m'sunagogemo anadzala ndi mkwiyo pakumva izi;

29. nanyamuka na mturutsira Iye kunja kwa mudziwo, nanka naye pamutu pa phiri pamene panamangidwa mudzi wao, kuti akamponye iye pansi.

30. Koma iye anapyola pakati pao, nacokapo.

31. Ndipo iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya, Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi ciphunzitso cace;

Werengani mutu wathunthu Luka 4