Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 4:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kucokera ku Yordano, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai.

2. Ndipo iye sanadya kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.

3. Ndipo mdierekezi anati kwa iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate.

4. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.

5. Ndipo m'mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m'kamphindi kakang'ono.

6. Ndipo mdierekezi anati kwa iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: cifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna.

7. Cifukwa cace ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.

8. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,Ambuye Mulungu wako uzimgwadira,Ndipo iye yekha yekha uzimtumikira,

Werengani mutu wathunthu Luka 4