Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 3:12-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizicita ciani?

13. Koma iye anati kwa iwo, Musakapambe kanthu konse kakuposa cimene anakulamulirani.

14. Ndipo asilikari omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizicita ciani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu ali yense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.

15. Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganizaganiza m'mitima yao za Yohane, ngati kapena iye ali Kristu;

16. Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zace; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

17. amene couluzira cace ciri m'dzanja lace, kuti ayeretse padwale pace, ndi kusonkhanitsa tirigu m'ciruli cace; koma mankhusu adzatentha m'moto wosazima.

18. Coteretu iye anauza anthu Uthenga Wabwino ndi kuwadandaulira zinthu zina zambiri.

19. Koma Herode mfumu ija, m'mene Yohane anamdzudzula cifukwa ca Herodiya, mkazi wa mbale wace, ndi ca zinthu zonse zoina Herode anazicita,

20. anaonjeza pa zonsezi icinso, kuti anatsekera Yohane m'nyumba yandende.

21. Ndipo panali pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo Yesu anabatizidwa, nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo,

22. ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lace ngati nkhunda, nadza pa iye; ndipo munaturuka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

23. Ndipo Yesuyo, pamene anayamba nchito yace, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Heli,

24. mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Melki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe,

Werengani mutu wathunthu Luka 3