Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:30-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.

31. Komatu tafuna-funani Ufumu wace, ndipo izi adzakuonjezerani.

32. Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; cifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.

33. Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zacifundo; mudzikonzere matumba a ndarama amene sakutha, cuma cosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

34. Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

35. Khalani odzimangira m'cuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

36. ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kucokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.

37. Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'cuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.

38. Ndipo akadza ulonda waciwiri, kapena wacitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.

39. Koma zindikirani ici, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yace yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yace ibooledwe.

40. Khalani okonzeka inunso; cifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa munthu akudza.

41. Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?

42. Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wace adzamuika kapitao wa pa banja lace, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yace?

43. Wodala kapoloyo amene mbuye wace pakufika, adzampeza alikucita cotero.

44. 1 Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo.

Werengani mutu wathunthu Luka 12