Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 1:9-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye m'Kacisi wa Ambuye.

10. Ndipo khamu lonse la anthu Iinalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira.

11. Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira ku dzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira.

12. Ndipo Zakariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira.

13. Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zakariya, cifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yohane.

14. Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwace.

15. Pakuti iye adzakhala wamkuru pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena, kacasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.

16. Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israyeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wao.

17. Ndipo adzamtsogolera iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.

18. Ndipo Zakariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ici ndi ciani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zace za mkazi wanga zacuruka.

19. Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, ine ndine Gabrieli, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.

20. Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzacitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mau, anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yace.

21. Ndipo anthu analikulindira Zakariya, nazizwa ndi kucedwa kwace m'kacisimo.

22. Koma m'mene iye anaturukamo, sanatha kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya m'Kacisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.

23. Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wace anamarizidwa, anamuka kunyumba kwace.

24. Ndipo atatha masiku awa, Elisabeti mkazi wace anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati,

25. Ambuye wandicitira cotero m'masiku omwe iye anandipenyera, kucotsa manyazi anga pakati pa anthu.

Werengani mutu wathunthu Luka 1